Numbers 35:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kapena munthu akamenya mnzake ndi chibonga choti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena akamkantha m'dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kapenanso ngati wina ali ndi chibonga mʼdzanja mwake choti nʼkupha nacho munthu, namenya nacho munthu, munthuyo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha, wakuphayo ayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena akamkantha m'dzanja muli cipangizo camtengo, cakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.