Numbers 35:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kapena kumpanda ndi dzanja lake modana naye, mnzakeyo naafa, ndiye kuti amene adamenya mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ndi wopha munthu ameneyo. Mbale wa munthu wakufayo ndiye aphe wopha mnzakeyo akangokumana naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena ngati, chifukwa cha udani, amenya mnzake ndi nkhonya, mnzakeyo ndi kufa, munthuyo ayenera kuphedwa. Iyeyo ndi wakupha. Wolipsira adzamuphe wakuphayo pamene akumana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena kumpanda ndi dzanja lace momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo pomkumika.