Numbers 35:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu munthuyo ayenera kukhala mu mzinda umene adathaŵiramo mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira. Koma mkulu wa ansembe onse atamwalira, wopha mnzakeyo angathe kubwerera ku dziko lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wolakwayo ayenera kukhala mu mzinda wopulumukiramowo mpaka imfa ya mkulu wa ansembe ndipo pamenepo atha kubwerera kwawo. Pokhapokha atafa mkulu wa ansembe ndi pamene angathe kubwerera ku malo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wace wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lace lace.