Numbers 35:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musaipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amaipitsa dziko, ndipo nkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa m'menemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene adakhetsa magaziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Musayipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amayipitsa dziko ndipo nʼkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa mʼmenemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko cifukwa ca mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.