Numbers 35:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mabusa a mizindayo amene mudzapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mzinda, adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Malo a msipu a mudziwo amene mudzawapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mudzi ndipo adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mudziwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono cikwi cimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja.