Numbers 35:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mukupatula mizinda imeneyi pa choloŵa cha Aisraele, muchotse mizinda yambiri pa mafuko aakulu, ndipo muchotse mizinda pang'ono pa mafuko aang'ono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa choloŵa chimene lalandira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mukupatula midzi imeneyi pa cholowa cha Aisraeli, muchotsepo midzi yambiri pa mafuko aakulu, ndipo midzi pangʼono pa mafuko aangʼono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa cholowa chimene lalandira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yao yao ya ana a Israyeli, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa colowa cao adacilandira.