Numbers 36:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri a banja la ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase, limodzi mwa mabanja a adzukulu a Yosefe, adabwera kudzalankhula ndi Mose ndi atsogoleri, akulu a mabanja a makolo a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri a mabanja a fuko la Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase omwe anali ochokera ku fuko la ana a Yosefe anabwera ndi kuyankhula ndi Mose, atsogoleri ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akuru a makolo a mabanja a ana a Gileadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akuru a makolo a ana a Israyeli;