Numbers 36:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adati, “Chauta adakulamulani inu mbuyathu kuti mutachita maere, mupatse Aisraele dziko, kuti likhale choloŵa chao. Ndiponso inu mbuyathu, Chauta adakulamulani kuti mupatse choloŵa cha mbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake akazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israyeli dzikoli mocita maere likhale colowa cao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ace akazi colowa ca Tselofekadi mbale wathu.