Numbers 36:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati akwatiwa ndi amuna a mafuko ena a Aisraele, choloŵa chao chidzachotsedwa pa choloŵa cha makolo athu ndi kuwonjezera pa choloŵa cha fuko la amuna aowo, motero choloŵa chathu chidzachepa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mapfuko ena a ana a Israyeli, acicotse colowa cao ku colowa ca makolo athu, nacionjeze ku colowa ca pfuko limene adzakhalako; cotero acicotse ku maere a colowa cathu.