Numbers 36:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zomwe Chauta akulamula za ana aakazi a Zelofehadi ndi izi: Aloleni akwatiwe ndi yemwe akumufuna, malinga akwatiwe ndi a m'banja la fuko la makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Cholamulira Yehova za ana akazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Colamulira Yehova za ana akazi a Tselofekadi ndi ici, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ace; komatu akwatibwe nao a banja la pfuko la makolo ao okha okha.