Numbers 36:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi aliyense amene alandira choloŵa m'fuko lililonse la Aisraele, akwatiwe ndi ana a abale a bambo wao. Mwisraele aliyense adzalandira choloŵa cha makolo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwana wamkazi yense wa mapfuko a ana a Israyeli, wakukhala naco colowa, akwatibwe ndi wina wa banja la pfuko la kholo lace, kuti ana a Israyeli akhale naco yense colowa ca makolo ace.