Numbers 4:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aikepo ziŵiya zonse zapaguwa zimene amagwiritsira ntchito pamenepo, monga zofukizira lubani, zitsulo zokoŵera nyama, zoolera phulusa ndi mabeseni, kungoti ziŵiya zonse za pa guwalo. Pa zonsezo ayalepo zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka aziyikapo zipangizo zonse zogwiritsira ntchito potumikira pa guwa, kuphatikizapo miphika yowotchera nyama, mafoloko otengera nyama, zowolera phulusa ndi mbale zowazira magazi pa guwa lansembe ndipo pamwamba pake aziyalapo zikopa za akatumbu ndi kuziyika mʼzonyamulira zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naikepo zipangizo zace zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zaolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zace.