Numbers 4:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aroni ndi ana ake, atamaliza kuphimba malo opatulika pamodzi ndi zipangizo zake zonse, pamene anthu akusamuka, ana a Kohati ndiwo abwere kudzanyamula zimenezi, koma asakhudze zinthu zopatulika, kuti angafe. Zimenezi ndizo zinthu za m'chihema chamsonkhano zimene ana a Kohati azinyamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatha Aroni ndi ana ake amuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati adze m'chihema chokomanako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Aaroni ndi ana ake aamuna akamaliza kukutira ziwiya za ku malo wopatulika ndi zipangizo zopatulika zonse, ndipo akakonzeka kusamuka pamalopo, Akohati abwere kudzazinyamula koma asagwire zinthu zopatulikazo. Akatero adzafa. Izi ndizo zinthu zimene Akohati ayenera kunyamula mu tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatha Aroni ndi ana ace amuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zace zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'cigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'cihema cokomanako.