Numbers 4:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa Kachisi opatulika, ndi zipangizo zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe, aziyangʼanira mafuta a nyale, ndi lubani wa nsembe zofukiza, nsembe yaufa yoperekedwa nthawi zonse ndi mafuta odzozera. Aziyangʼaniranso chihema ndi zonse zili mʼmenemo, kuphatikizapo zida ndi ziwiya zonse zopatulika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa kacisi wonse, ndi zonse ziri m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zace.