Numbers 4:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuti Akohatiwo asafe, akayandikira zinthu zopatulika kopambana, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe, ndipo apatse aliyense mwa Akohatiwo zoti achite ndi zoti anyamule.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake amuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma muziwachitira izi kuti asafe, akhalebe ndi moyo pamene ayandikira zinthu za ku malo wopatulika kwambiri: Aaroni ndi ana ake aamuna azipita ku malo wopatulika ndi kumamupatsa munthu aliyense ntchito yake ndi zimene ayenera kunyamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulikitsazo; Aroni ndi ana ace amuna alowe, namuikire munthu yense nchito yace ndi katundu wace.