Numbers 4:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azinyamulanso nsalu zochingira bwalo, nsalu yochingira khomo la pa chipata cha bwalo lozungulira malo opatulika ndi guwa, zingwe zake ndi zipangizo zina zonse zofunika. Agwire ntchito zonse zimene aŵapatse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsalu zochingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa Kachisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
makatani wotchingira bwalo lozungulira chihema ndi guwa, katani ya pa khomo, zingwe ndi zida zonse zimene zimagwiritsidwa ntchito mʼchihema. Ageresoni azichita zonse zofunika kuchitika ndi zinthu zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsaru zocingira za pabwalo, ndi nsaru yotsekera ku cipata ca pabwalo liri pakacisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za Debito zao, ndi zonse acita nazo; m'menemo muli nchito zao.