Numbers 4:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene aziyang'anira ntchito zonse za ana a Ageresoni, ndi Aroni pamodzi ndi ana ake. Aziyang'anira zonse zimene ayenera kunyamula, ndi zonse zimene ayenera kuchita. Ndinu amene mudzayenera kuŵafotokozera udindo wa kunyamula zonse zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito yawo yonse, kaya kunyamula kapena kugwira ntchito zina, achite Ageresoni motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Uwagawire ntchito zonse zimene akuyenera kugwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nchito yonse ya ana a Agerisoni, kunena za akatundu ao ndi nchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ace amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse.