Numbers 4:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene iwo alamulidwa kuti anyamule pa ntchito yao ya m'chihema chamsonkhano nazi: anyamule mitengo ya malo opatulika monga mafulemu ake, mizati yake ndi masinde ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako ndi ichi: matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito yawo pamene azikatumikira mu tenti ya msonkhano ndi iyi: kunyamula matabwa a chihema, mitanda, mizati ndi matsinde,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako ndi ici: matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace;