Numbers 4:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anyamulenso mizati yozungulira bwalo, pamodzi ndi zikhomo zake, zingwe zake, kudzanso zipangizo zake zonse, ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Poŵauza zinthu zimene aliyense ayenera kunyamula, uzitchula chinthu chilichonse chimodzichimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso mizati yozungulira bwalo ndi matsinde ake, zikhomo za chihema, zingwe ndi zipangizo zake zonse ndiponso zonse zokhudzana ndi ntchito yake. Uwuze munthu aliyense chomwe ayenera kuchita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsici za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace, pamodzi ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito yace yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwaehula maina ao.