Numbers 4:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imeneyi ndiyo ntchito ya mabanja a ana a Merari, ndipo ntchito yao yonse ya m'chihema chamsonkhanoyo, aziiyang'anira ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyi ndiyo ntchito ya mafuko a Amerari pamene akugwira ntchito ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Itamara mwana wa wansembe Aaroni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iyi ndi nchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa nchito zao zonse m'cihema cokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe.