Numbers 4:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimenecho ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'mabanja a Akohati, onse amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ichi chinali chiwerengero cha mafuko a Akohati onse omwe ankatumikira mu tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'cihema cokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.