Numbers 4:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimenechi ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'banja a Ageresoni, amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Geresoni, onse akutumikira m'chihema chokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ichi chinali chiwerengero cha Ageresoni mwa mabanja awo amene ankatumikira ku tenti ya msonkhano. Mose ndi Aaroni anawawerenga monga mwa lamulo la Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Gerisoni, onse akutumikira m'cihema cokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.