Numbers 4:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adaŵasankha kuti ena azigwira ntchito yotumikira, ndipo ena azinyamula katundu, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Umu ndimo m'mene adaŵaŵerengera anthuwo, monga momwe Chauta adaamlamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense anamupatsa ntchito ndi kumuwuza choti anyamule monga mwa lamulo la Yehova kudzera mwa Mose. Anawawerenga chomwechi potsata zimene Yehova analamula Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.