Numbers 5:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwamuna wina atachita naye chigololo, zimenezo zitha kubisika, mwamuna wake osazidziŵa. Mkaziyo atha kukhala wosazindikirika kuti wadziipitsa, chifukwa chosoŵa mboni yomtsutsa, popeza kuti sadampezerere akuchita kumene.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita),
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wace, ndikumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwira alimkucita;