Numbers 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mwamunayo abwere ndi mkazi wakeyo kwa wansembe. Ndipo aperekere nsembe ya ufa wabarele wokwanira kilogaramu limodzi. Asathirepo mafuta kapena lubani pa nsembeyo, poti ndi chopereka cha chakudya choperekera nsanje, nsembe yotsutsa munthu, yoperekedwa kuti tchimo lakelo lizidziŵika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
apite naye mkaziyo kwa wansembe. Ndipo popita atengenso gawo lakhumi la chopereka chaufa wa barele wokwana kilogalamu imodzi mʼmalo mwa mkaziyo. Asathire mafuta pa nsembeyo kapena lubani, chifukwa ndi nsembe ya chopereka ya chakudya yopereka chifukwa cha nsanje, nsembe yozindikiritsa tchimo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wace kwa wansembe, nadze naco copereka cace, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo libano; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yacikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.