Numbers 5:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkaziyo amuimike pamaso pa Chauta ndi kummasula tsitsi, ndipo aike m'manja mwake nsembe yaufa yachikumbutso, chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Wansembeyo atenge madzi oŵaŵa m'manja mwake, madzi odzetsa matemberero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe atayimika mkaziyo pamaso pa Yehova, amumasule tsitsi lake, ndipo ayike mʼmanja mwake nsembe yozindikiritsa tchimo, nsembe yachakudya ya nsanje, wansembeyo atanyamula madzi owawa omwe amabweretsa temberero.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Mulungu, nabvula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yacikumbutso m'manja mwace, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwace mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.