Numbers 5:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amlumbiritse mkaziyo kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sadagone nawe, ndipo ngati sudachite kanthu kokuipitsa pamene unali m'manja mwa mwamuna wako, madzi oŵaŵa ali apaŵa usatenge nawo matemberero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka wansembeyo alumbiritse mkaziyo ndi kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sanagonane ndi iwe ndipo sunayende njira yoyipa ndi kukhala wodetsedwa pomwe uli pa ukwati ndi mwamuna wako, madzi owawa awa omwe amabweretsa temberero asakupweteke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagona nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kucidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.