Numbers 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Lamula Aisraele kuti achotse wakhate aliyense m'zithando, aliyense wotulutsa zinthu zoipa m'thupi mwake, ndiponso munthu wodziipitsa pokhudza mtembo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi odetsedwa chifukwa cha akufa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lamula Aisraeli kuti achotse mu msasa aliyense amene ali ndi matenda opatsirana a pa khungu kapena matenda otuluka madzi mʼthupi a mtundu uliwonse, kapena aliyense wodetsedwa chifukwa cha munthu wakufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Uza ana a Israyeli kuti aziturutsa m'cigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa cifukwa ca akufa;