Numbers 5:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(apo wansembeyo amlumbiritse mkaziyo ndi mau amatemberero, ndi kumuuza kuti), ‘Chauta alisandutse dzina lako matemberero pakati pa anthu a mtundu wako Chauta afwapitse m'chiwuno mwako, ndi kutupitsa thupi lako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo wansembe alumbiritse mkaziyo ndi mawu a matemberero ndi kumuwuza kuti, ‘Yehova achititse anthu ako kukutemberera ndi kukunyoza pamene awononga ntchafu yako ndi kutupitsa mimba yako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'cuuno mwako, ndi kukutupitsa mbulu;