Numbers 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muchotse anthu onse otere, amuna kapena akazi. Muziŵatulutsira kunja kwa zithando kuti angaipitse zithando zao, poti Ine ndimakhala pakati pa anthu anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muchotse amuna komanso amayi ndipo muwatulutsire kunja kwa msasa kuti asadetse msasa wawo kumene Ine ndimakhala pakati pawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
muwaturutse amuna ndi akazi muwaturutsire kunja kwa cigono, kuti angadetse cigono cao, cimene ndikhala m'kati mwacemo.