Numbers 5:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
kapena mwamuna akayamba kuchitira mkazi wake nsanje ndipo akumganizira zoipa. Mwamunayo amuimike mkazi wake pamaso pa Chauta, ndipo wansembe amchitire monga momwe lamulo likunenera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena pamene maganizo a nsanje abwera kwa mwamuna wake chifukwa chokayikira mkazi wakeyo. Wansembe azitenga mkazi wotere ndi kumuyimiritsa pamaso pa Yehova ndipo agwiritse ntchito lamulo lonseli kwa mkaziyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo acitira mkazi wace nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amcitire cilamulo ici conse.