Numbers 5:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu akapanda kukhala ndi wachibale woti nkulandira zinthu zobwezedwa zija m'malo mwa zoonongedwazo, apereke zobwezedwazo kwa Chauta kuti zikhale za wansembe, kuwonjezera pa nkhosa yamphongo yadipo ija imene amachitira mwambo wopepesera machimo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wolakwiridwayo alibe mʼbale komwe kungapite zinthu zobwezedwazo, zinthuzo zikhale za Yehova ndipo azipereke kwa wansembe, pamodzi ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopepesera tchimo lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere coparamulaco, coparamula acibwezera Yehovaco cikhale ca wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya cotetezerapo, imene amcitire nayo comtetezera.