Numbers 6:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembeyo apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Tsono amchitire mwambo wopepesera machimo ake, chifukwa adalakwa poyandikana ndi mtembo. Tsiku lomwelo aperekenso tsitsi lake kwa Chauta,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anachimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wake tsiku lomwelo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yaucimo, ndi yina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anacimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wace tsiku lomwelo.