Numbers 6:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mwiniwakeyo akhale wake wa Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. Tsono abwere ndi mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti aperekere nsembe yopepesera kupalamula. Koma masiku a kudzipereka kwake koyamba kuja asaŵerengere, chifukwa kudzipereka kwakeko adakuipitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwace, nadze nayo nkhosa yamphongo ya caka cimodzi ikhale nsembe yoparamula; koma masiku adapitawa azikhala cabe, popeza anadetsa kusala kwace.