Numbers 6:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Lamulo la Mnaziri pamene nthaŵi ya kudzipereka kwake yatha, nali: abwere naye pakhomo pa chihema chamsonkhano,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chilamulo cha Mnaziri, atatha masiku a kusala kwake ndi ichi: azidza naye ku khomo la chihema chokomanako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cilamulo ca Mnaziri, atatha masiku a kusala kwace ndi ici: azidza naye ku khomo la cihema cokomanako;