Numbers 6:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo iye apereke mphatso zake kwa Chauta. Apereke mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi wopanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza. Apereke nkhosa imodzi yaikazi ya chaka chimodzi yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa imodzi yamphongo yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yachiyanjano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo abwere naco copereka cace kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya caka cimodzi yopanda cirema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yamsoti yopanda cirema ikhale nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda cirema ikhale nsembe yoyamika;