Numbers 6:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero, apereke nkhosa yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yachiyanjano, pamodzi ndi dengu la buledi uja wosafufumitsa. Kenaka aperekenso chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi mtanga wa mkate wopanda cotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.