Numbers 6:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mnaziriyo amete kumutu kwake koperekedwa kuja pakhomo pa chihema chamsonkhano. Ndipo atenge tsitsi la ku mutu wake woperekedwawo, ndi kulitentha pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wace wa kusala kwace pa khomo la cihema cokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wace wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.