Numbers 6:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe atenge mwendo wamwamba wa nkhosa yamphongo wophika, ndipo atengenso keke imodzi yosatupitsidwa, pamodzi ndi mtanda umodzi wa buledi wosatupitsidwa, ndipo aziike m'manja mwa Mnaziri, atameta tsitsi lake loperekedwa lija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa ka m'dengu, ndi kamtanda kaphanthi kopanda chotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda cotupitsa ka m'mtanga, ndi kamtanda kaphanthi kopanda cotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwace;