Numbers 6:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo wansembeyo azipereke moweyula, kuti zikhale nsembe zoweyula pamaso pa Chauta. Zimenezi nzoyera, zokhalira wansembe, pamodzi ndi nganga yoperekedwa moweyula ija. Pambuyo pake Mnaziri angathe kumwa vinyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ici ncopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.