Numbers 6:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Limeneli ndilo lamulo la munthu amene alumbira kuti akhale Mnaziri. Zinthu zake zimene apereka kwa Chauta zikhale zomwe adalumbirira pa unaziri, osaŵerengera zina zimene angathe kupereka moonjezerapo. Zimene adalumbira kuti adzachita, achite momwemo potsata lamulo la kudzipereka kuti adzakhale Mnaziri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ici ndi cilamulo ca Mnaziri wakuwinda, ndi ca copereka cace ca Yehova cifukwa ca kusala kwace, pamodzi naco cimene dzanja lace likacipeza; azicita monga mwa cowinda cace anaciwinda, mwa cilamulo ca kusala.