Numbers 6:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Asamwe vinyo wopangidwa ndi mphesa kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo asamwe madzi amphesa kapena kudya mphesa zaziŵisi kapena zouma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
azisala vinyo ndi kacasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kacasu wosasa, kapena cakumwa conse ca mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.