Numbers 6:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa masiku onse amene adalumbira kuti adzakhala wodzipereka kwa Chauta, asamete kumutu kwake ndi lumo. Adzakhale wake wa Chauta nthaŵi zonse mpaka atatha masiku ake odzipereka kwa Chauta. Alilekerere tsitsi lake kuti likule.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku onse a cowinda cace cakusala, lumo lisapite pamutu pace; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lace zimeretu.