Numbers 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asadziipitse poyandikira mtembo wa bambo wake, wa mai wake, wa mbale wake kapena wa mlongo wake, chifukwa kulumbira kwa kudzipereka kwake kwa Mulungu kuli pamutu pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Asadzidetse ndi atate wace, kapena mai wace, mbale wace, kapena mlongo wace, akafa iwowa; popeza cowindira Mulungu wace ciri pamutu pace.