Numbers 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, ndi beseni lasiliva limodzi lowazira, lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo wopatulika ndipo zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka chachakudya;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembeyaufa;