Numbers 7:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zisanu zamphongo, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Netanele mwana wa Zuwara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Netanele mwana wa Zuwara.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi, nsembe ya chiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Netanieli mwana wa Zuwara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Netaneli mwana wa Zuwara.