Numbers 7:71 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahiyezere mwana wa Amishadai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahiyezeri mwana wa Amisadai.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Ahiyezeri mwana wa Amisadai.