Numbers 7:77 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Pagiyele mwana wa Okarani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Pagiyele mwana wa Okarani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Pagieli mwana wa Okirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Pagiyeli mwana wa Okirani.