Numbers 7:79 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;