Numbers 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Merari adaŵapatsa ngolo zinai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu potsata ntchito yao, imene woyang'anira wake anali Itamara, mwana wa wansembe Aroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiponso anapereka ngolo zinayi ndi ngʼombe zothena zisanu ndi zitatu kwa Amerari molingananso ndi ntchito yawo. Onsewa ankawayangʼanira anali Itamara mwana wa Aaroni wansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napatsa ana a Merari magareta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa nchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.